Mabugwe omwe siaboma m`boma la mchinji ati ndikofunika kuti anthu adzitenga nawo gawo pakuyendetsedwe kazitukuko zomwe zikuchitika m`bomali
Malingana ndi wachiwiri Wamkulu wabungwe omwe siaboma m`bomali aDavis Damson, wati nzika zomwe ziyenerera kupindula pazitukuko ngati zitenga nawo gawo pakayendetsedwe kazitukuko zithandiza kuti zinkazi zidzivomereza ntchito zomwe zikuchitika .
Ndipo ati ngati zitukuko ziyendetsedwa komanso kuyang`aniridwa ndi makomiti oyendetsa zitukuko m`madera, zipangitsa kuti zithu zidzichitika poyera.
A Damson ati ndikofunikira kuti khosolo yam`boma la mchinji ilimbikitse ntchito zamakomitiwa.
Padakali pano, mabugwe omwe siaboma akhala akuyenderanso ntchito zachitukuko zomwe zikuchitika pansi pa GESD m`bomali.
Zotsatira pakuyendera kuyamba , zawonetsa kuti zitukuko zina zinachitika popanda makomiti oyendetsa azachitukuko.