Bungwe la MACOKASA lati anthu onse oyendetsa njinga zamoto atatsatira ndondomeko yomwe boma layamba pa kalembera wa ziphaso za njinga zamoto ndi zoyendetsela zithandiza kuchepetsa ngozi zapamseu ndi upandu mudziko muno.
Wapampando wa bungwe la MACOKASA, Moses Mwalabu wayankhula izi ku pa msika wa Kamwendo ku Mchinji pamsokhano wowadziwitsa anthu za ndondomekoyi.
Ndondomeko ya Kulembetsa kwa njinga zamoto ndi kupereka ziphaso lomwe limazike pa June 30, 2025 ithandiza oyendetsa njinga zamoto kukhala ndi chitetezo chokwanira.
Iwo ati aliyense amene alephere kutsatira kalembera wa njinga zamoto womwe ukuchitika adzalandira chilango.
Iwo ati akuyembekezera kuti oyendetsa njinga zamoto okwana 5 Million akhala maembala abugwe la MACOKASA
Wapampando wapolisi ya mudzi ya pakwamwendo a Ishmael Mdoka wati kalemberayo uthandiza oyendetsa njinga zamoto kutsatira malamulo apamseu ndikuchepetsa ngozi za pamseu..