Wolemba: Vester Chunga
Mkulu wa bwalo loweruza milandu m’bomali , A Fred Juma Chilowetsa anati ngati anthu azitsatira malamulo oteteza ana ziwapangitsa kusiya kuchitira nkhanza ana komanso ana adzilandira chithandizo choyenera ngati achitiridwa nkhaza.
Iwo anati dziko la Malawi likuyenera kuti linakwanilitse kukhazikitsa ndondomeko zonse zomwe zili muli lamulo loteteza la ana la Child Care and protection justice act kuti ana asiye makhalidwe a kuba ndi upandu.
Izi zanenedwa lolemba, pamsokhano omwe bugwe la Girls Activists Youth organization ( GAYO) linachititsa pa bwalo lazamasewero la sukulu yapulayimale ya Chakhanga kwa mfumu yayikulu Kapondo ,m`bomali okhudza malamulo ndi chitetezo cha ana.
Isabelo Jere , Woona za ma pologalamu ku bugwe la Girls Activists youth organization wapepha adindo m`madera kuti akuyenera kukhazikitsa magulu oyang`anira chitetezo cha ana komanso kukhala patsogolo kuphunzitsa anthu za ubwino oteteza ana ndi kutsatira malamulo.