Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority MACRA lati ndilodzipereka kuteteza maufulu a nthu ogula katundu.
M’modzi mwa membala wa board ya MACRA a Stella Chiithi anena izi lachiwiri ku Deira Lodge mboma la mchinji pa mwambo okumbukira tsiku la ogula la World Consumer Rights pachingerezi.
Mkulu wa bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) Executive Director, Lloyd Vincent Boma ati pakufunika mgwirizano wabwino pakati pa bungwe al MACRA ndi mabungwe ena ndikuti athane ndi mavuto a kuberedwa ndalama ndi milandi ya pa intaneti.
Polankhula pa mwambowu, A Chuthi atsindika kufunika koti anthu ogula katundu azikanena ku bungweri ngati sanathandizidwe moyenera ndi makampani monga Airtel Malawi ndi TNM kutibungweri lizichitapo kanthu.
Iwo apempha nzika za dziko lino kuti zipewe kufalitsa uthenga wa bodza kupatula kuti iwo akudziwa Ufulu wawo.
Iwo awonjezera kuti bungweri lilimbitsa chitetezo chokhidza internet ndikuti ateteze anthu kubweredwa kudzera pa intaneti ndi ma foni a m’manja.
Mkulu wa bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC), a Lloyd Vincent Nkhoma awuza ogula kuti akhale ndi udindo odziteteza poberedwa ndalama pa foni ndi milandu yokhudza intaneti.
Tsikuli lomwe limakumbukiridwa pa 15 Marich pa dziko lonse, limakumbukiridwa pa mutu oti “kukhazikitsa malo abwino amakono kwa anthu ogula.”
Mwambowu unabweretsa pamodzi ogula, akulu akulu kuchokera ku bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC), gulu la ICT Association of Malawi, MACRA, banki yayikulu ya Reserve mwa ena.