KHOSOLO YA MCHINJI IPEREKA MADZI ABWINO

Ngati njira imodzi yoonetsetsa kuti anthu okhala m’boma la Mchinji akugwiritsa ntchito madzi aukhondo maka m’madera a Mfumu yayikulu Nyoka komanso Zulu, khosolo ya boma la Mchinji lakhazikitsa pulojekiti imene ikutenga madzi kuchoka mphiri la Mchinji kudzera mma payipi kupita m’madera osiyanasiyana.

Ntchito yochotsa madzi kuchoka mphiri la Mchinji idayima m’chaka cha 2000 kaamba koti zipangizo zina zimene zimagwiritsidwa ntchito popopa madziwa zinaonongeka.

Kuchoka mchaka cha 2000 kufika pano anthu a m’madera a mfumu yayikulu Nyoka komanso Zulu akhala akugwiritsa ntchito madzi ochoka m’zitsime amene samakhala otetekeza kutizilombo timene timayambitsa matenda otsekula m’mimba.

Malingana ndi Nkulu wonyang’anira zitukuko pansi pa khosolo ya boma la Mchinji, a Martin Pindankono ati khosoloyi yabweretsa chitukukochi poona mavuto a madzi aukhondo m’maderawa zimene zimadzetsa matenda osiyanasiyana.

Komabe a Pindankono apempha anthu amene apindulire ndi chitukukochi kuti asamalire zipangizo zonse zomwe zithandizire kutenga madzi kuchoka ku phiri la Mchinji kupita ku madera awo.

Chitukuko chochotsa madzi kuphiri la Mchiji ndi gawo limodzi la zitukuko zosiyanasiyana zimene kholoso la boma la Mchinji likuchita pansi pa pulojekiti ya Government to Enable Service Delivery (GSED) yomwe ndiya ndalama zokwana 1.1 billion kwacha.

Related posts

MACRA ITETEZE UFULU WA ANTHU PA INTERNET

ADINDO APEMPHA ANTHU KU MCHINJI KUTSATIRA MALAMULO OTETEZA MAUFULU A ANA.

MACOKASA LATI ANTHU ONSE OYENDETSA NJINGA ZAMOTO ATATSATIRA MALAMULO