ADINDO APEMPHA ANTHU KU MCHINJI KUTSATIRA MALAMULO OTETEZA MAUFULU A ANA.

Wowona za mapologalamu ku Gayo : Isabel Jere

Wolemba: Vester Chunga

Mkulu wa bwalo loweruza milandu  m’bomali , A  Fred Juma Chilowetsa anati ngati anthu azitsatira malamulo oteteza ana ziwapangitsa kusiya kuchitira nkhanza ana komanso ana  adzilandira chithandizo choyenera ngati achitiridwa nkhaza.

Iwo anati dziko la Malawi likuyenera kuti linakwanilitse kukhazikitsa  ndondomeko zonse zomwe zili muli lamulo loteteza la ana la Child Care and protection justice act kuti ana asiye makhalidwe a kuba ndi upandu.

Izi zanenedwa lolemba, pamsokhano omwe bugwe la Girls Activists Youth organization ( GAYO) linachititsa pa bwalo lazamasewero  la sukulu yapulayimale ya Chakhanga kwa mfumu yayikulu Kapondo ,m`bomali okhudza malamulo ndi chitetezo cha ana.

Isabelo Jere , Woona za ma pologalamu ku bugwe la Girls Activists youth organization wapepha adindo m`madera kuti akuyenera kukhazikitsa  magulu oyang`anira  chitetezo cha ana komanso kukhala patsogolo  kuphunzitsa anthu za ubwino oteteza ana ndi kutsatira malamulo.

Related posts

MACRA ITETEZE UFULU WA ANTHU PA INTERNET

KHOSOLO YA MCHINJI IPEREKA MADZI ABWINO

MACOKASA LATI ANTHU ONSE OYENDETSA NJINGA ZAMOTO ATATSATIRA MALAMULO