MABUGWE OMWE SIABOMA KU MCHINJI ATI NDIKOFUNIKA KUTI ANTHU ADZITENGA NAWO GAWO

Mabugwe omwe siaboma m`boma la mchinji ati ndikofunika kuti anthu adzitenga nawo gawo pakuyendetsedwe  kazitukuko zomwe zikuchitika m`bomali

Malingana ndi wachiwiri Wamkulu wabungwe omwe siaboma m`bomali aDavis Damson, wati nzika zomwe ziyenerera kupindula pazitukuko  ngati zitenga nawo gawo pakayendetsedwe kazitukuko zithandiza kuti  zinkazi zidzivomereza ntchito zomwe zikuchitika .

Ndipo ati ngati zitukuko ziyendetsedwa komanso kuyang`aniridwa ndi makomiti oyendetsa zitukuko m`madera, zipangitsa kuti zithu zidzichitika poyera.

A Damson ati ndikofunikira kuti khosolo yam`boma la mchinji ilimbikitse ntchito zamakomitiwa.

Padakali pano, mabugwe omwe siaboma akhala akuyenderanso ntchito zachitukuko zomwe zikuchitika pansi pa GESD m`bomali.

Zotsatira pakuyendera kuyamba , zawonetsa kuti zitukuko zina zinachitika popanda makomiti oyendetsa azachitukuko.

Related posts

MACRA ITETEZE UFULU WA ANTHU PA INTERNET

ADINDO APEMPHA ANTHU KU MCHINJI KUTSATIRA MALAMULO OTETEZA MAUFULU A ANA.

KHOSOLO YA MCHINJI IPEREKA MADZI ABWINO